![]() |
Soldier of Christ Disciple Training Ministries |
|
MAKIYI A ZIFANIZO ZONSE - MARKO 4:13 |
|
| Pafupi zaka 2000 tiku phunzira baibuio nthano mbiri ndi machenjezo komabe osava. Kumba marko 4-3. Yesu anayamba kuphunzitsa za fanizola ofesa akufesa panthaka Zosiyana Atamaliza fanizoanawafunsa, ngati simumvetsa fanizo ili, Kodi mudzamvetsa bwanji mafanizo ena? M’mau ake yesu, fanizo ili ndilo makiyi okamvetseta mafanizo onse. Fanizo lili ndi zinsinsi zoiwalika zomwe zinatsekededwa pofuna kutsitwimutsa mipingo yathu yakufa,pa chikhalidwe chathu chufunda osatentha – kapena kuzizila zopanda ntchito zoyembeka kusanzidwa ndi Mulungu. Tiyeni tione fanizo, lanenedwa mumauthenga atatu: Aliyense akuwonjezera pa nkhaniyi ndiye tawaphatikiza kuti tione pamodzi palibe kusintha kuti tisaononge mbali iliyiyonse. Kuchkera Marko 4:3-9 Luke 8:5-8 Mateyo 13:3-9. Ofesa, anatuluka kukafesa mbewu, ndipo anafesa, zina zinagwera mbali mwa nsewu zinapondedwa, komanso mbalame za mulengalenga zinadya. Zina zinagwera pa miyala popanda dothi lochuluka, ndipo zimera, koma chifukwa chopanda dothi lochuluka, zitakula, dzuwa litawala, zinapselera, chifukwa zinalibe chinyezi komanso mizu. Mbewu zina zinagwera pa minga, ndipo zinatchingidwa, ndipo sizinabala zipatso. Mbewu zinagwera pa nthaka ya bwino pamene zinakula zina chula komanso kubala zipatso zochuluka kwambiri. Tisanaonjezere tiyeni tione mmene Yesu Khristu analongosolera fanizoli, komanso kuchokera kuyankho lake la sakanizidwanso kuchokera mu Mark 4:14-20 luke 8: 11-15 ndi Mateyo 13: 18-23. Ndipo iye anati Kodi simudziwa fanizoli? Mudzazindikira bwanji ena? Nali fanizoli: Ofesa mbewu ndipo mbewu ndi mau a Mulungu. Zogwera mbali mwa mseu ndi anthu ena amene anamva uthenga koma osamvetsetsa mosachedwa mdyerekezi ndikutenga mau amene afesedwa mu mtima, kuti asakhulupilire ndi kupulumutsidwa. Chimodzimodzi zogwera pa miyala, amamva mau ndi kuwalandira mwachimwemwe. Amangokhulupilira mwakanthawi koma chifukwa alibe mizu ya mphamvu. Pakafika ziphinjo chifukwa cha mau, nthwawi amagwa, ena munthawi ya mayesero, amagwa. Mbewu imene inagwera pa minga, awandiamene amva mau koma amakula mmau, zosangalatsa zamoyo, ndipo mau amakhala opanda zipatso zoti zingakwime. Koma zogwera pamnthaka yabwino ndi kunetsetsa ndikuwasunga ndi kubala zipatso mopilira, ndikubweletsa mber zochuluka. Ndiye tidzifunse mafunso kuti timvetsetse. 1. Kodi zikulongosola chiani? Zophweka, fanizoli likukamba za kutembenuka mtima koona ndilinyenga tikiphunzira mmene tingawadziwile otembenuka eni eni. Komanso kwa mmene tinga dzalire mbewu. 2. Ofesa ndindani? Ofesa ndi Avangeli, Alaliki ndi wina aliyense amene amagawa uthenga kea otayika. Ndichimodzidzi uthenga kuuthenga kwa ofesa ndi kwa otayika. Ndife amene timamwanza uthenga mmalo mosiyana ndi kwa otayika. Ndife amene timamwanza uthenga mmalo mosiyana siyana. 3. Kodi nthaka ikuyimira ndani? Nthaka zinayi zikuyimira mitundu ina ya anthu. Komanso kutengera mitima yawo. Anthuwa ali mmagulu anai amene akuwasiyanitsa, malingana ndi momwe amawalandilira mau Amulunga. Chomwe tingaulure ndichakuti ena amakhala ndi mitima youma yosakonzeka kulandira mau. Ena amamva uthenga olakwika, kapena osatsiliza, ena amamva uthenga wabwino koma alephera kudziwa kudziwa dipo lake. Lachinayi, limamva kumvetsetsa ndi kukhala ndiuthenga. 4. Kodi zikutiuza Chiani Izi zikutengera Gulu limene inuyo muli. Ena mwaife ndiotayika ndi ofunika uthenga. Ena akukhala mubodza kudzimiza okha, komanso choonadi alibe. Amenewa ayenera kulingalira okha zimenezi. Ena, amene abala zipatso ayenera kusamalitsa kuopsa kwa uthinga wobwera kwa iwo kuti awonjezere zipatso osati aphumnthwe, munjira ina. 5. Kodi Zithandiza bwanji kutsegula zifanizo zina? Tiona kuti zifanizo zina zikukamba nkhani imodzi… kusiyanitsa pakata pa zeni zeni ndi zachinyengo. Zifanizo zambili mbaibulo zikukamba za otayika ndi opulutsidwa. Tikamvetseta chifanizochi koyamba tiona kuti zinazo zukukamba za kusiyana kwa Ana eni eni a Mulungu ndi ana achinyengo. Tione kufunika kwa makiyi pa zifanizo zonse. Tiyamba ndi mtundu ndi mtundu. Taonani kugwirizana kwa nkhani ya Yesu ndi kulongosola kwake monga talongosola. GAWO 1 - MBEWU ZA MPHEPETE MWA NSEWU. Fanizo: Ofesa anapita kukafesa, a kufesa, zina zinagwera mphepete mwa njira ndikumapondedwa ndi mapazi ndi mbalame za mulengalenga zina zidya. Kulongosola kwa Yesu: Ofesa nafesa mbewu ndipo mbewu ndi mau a Mulungu, zogwera mmbali mwamseu ndi amene amva uthenga koma osaumvetsa, mosachedwa mdyerekezi anabwera ndi kutenga mau amene afesedwa mumtima mwao, kuti asakhulupirire ndikupulumuka. Zolingalira: Anthu amene akunenedwa aa anawatchulapo pamene anali ku phunitsa ifanizo. Onani yankholalitali pa Mateyo 13: 11-17. Yesu anagwilitsa uneneri wa Yesaya 6:9-10 zokhudzana ndi anthu amene azolowera kuswa malamulo komanso kulekelera pa mau a Mulungu, komanso uzimu wawo wasokonekera, makutu awo atsekedwa ndi uchimo komanso maso awo aphimbidwa kuti asamve kapena kuona Ambuye, chilamulo kapena m’mene ayiniake (munthu) aliri. Tikupenzamo nkhani yomweyi pa Masalimo 119: 70, zikundiganizitsa zawina amene machubu amumtma wake atseka chifukwa cha mafuta amthupi kuti magazi asutse, koma zingathe kumupha. Ichi chinali chikhalidwe cha Ayuda, Aneneri onse anali ndi uthenga ofanana monga Zakariya 7: 11-12 Komanso Paulo pouza Timoteo pa 2 Timoteo 4:3-5. Tikaona avangeli …. Ofesa ….. kumwaza mbewu mbali mwansewu ndi awulesi ndi mnjira yo phweka. Tiyenera kukhala ndi nthawi yochoka mbali mwa msewu ndikupeza malo abwino. MBEWU ZA PAMIYALA (NTHATHWE) CHIFANIZO: Zina sinagwera pa miyala, ndipozinalibe dothi lambili ndipo zinamera koma chifukwa chopanda dothi lakuya, zitakula dzuwa nci kuwala zinapselera chifukwa chowa chinyezi komanso mizu. Yesu kulongosala: chimodzimodzi, zogwera pamiyala, amamva mau ndipo amawandira mwa chimwemwe, amakhulipilira mwa kamphindi koma chifukwa chowa mizu ya mphanvu, samakhazikika, pamene pabwera zobvuta chifukwa cha mau amagwa, ena munthawi ya zolingalira: Tione mfundo zina zokhumudzana ndi otembenuka – opa mnthala ya miyala kuti iye anafika otero bwanji. * Amamva mau ndipo nthawi yomweyo amalandira mwa chimwemmwe * Amangokhulupira kwa kanthawi * Amafota chifukwa (a) alibe mizu mkati mwake (b) komanso kusowa chinyezi amagwa nthawi yomweyo chifukwa cha mabvuto. |
|