Soldier of Christ Disciple Training Ministries
A ministry of Acts III Global Ministries – USA & Malawi – www.God.mw

Lesson 104

Kutsiliza kwake ndi funso “kodi ufumu wakumwamba ukuthanthauza chani. Kwa ongoyamba kumene mau oti ufumu wakumwamba akupezeka kokwana 32 mu baibulo lonse, komanso onsewa ali mu Mateyo! Uwu ndi uthenga omwewo umene ukutiuza kuti Yesu akupeleka kwa ife. Mafungulo a ufumu wa ku mwamba. Ndiye choyamba tifunse mmene mawuwa agwilitsa dwira nchito mu Mateyo.

Koyamba akupezeka ndi Yohane Mbatizi akuti “ Tembenukani mtima chifukwa ufumu wa kumwamba wayandikira” Apa ndi pa mateyo 3:2 pa mateyo 4:17 ndi pamene mauwa akupezeka kachiwiri yesu akuyankhula za mau omwewa” Kuyambira pamene yesu anayamba kulalikira ndi kunena” Tembenukani mitima pakuti ufumu wa kumwamba wayandikira” iyi inali nthawi imene Yohane ataponyedwa mndende.

Pa mateyo 5:3 Yesu anayamba ulaliki wake ndi mau awa “ Odala ali osauka muuzimu chifukwa wao ufumu wa kumwamba uthenga umeneu ukukamba za njira zisanu ndi zitatu zimene anthu adzadalitsikire. Izi ndi ndizofunikira kwambiri komaso akumaliza za kudalitsa kumeneku ndi mau awa “ Odala ali akuzunzudwa chifukwa cha chilungamo chifukwa uli wawo ufumu wa kumwamba Mateyo 5:10
M’malo ambiri mmene mauwa agwilitsidwa ntchito, akuwuza anthu mmene angolowere komanso kulephera kulowa mu ufumu wa kumwamba Mmalonso ambiri Yesu amagwilitsa ntchito mau omwewa poyamba zifanizo monga “ufumu wa kumwamba uli ngati_ _ _ _ _ _ kenaka amaphunzitsa pogwiritsa ntchito zitsanzo zakuthupi ndi kulumikiza ndi Uzimu. Chitsanzo chimodzi kuchokera pa Mateyo 13:47-50 “Ndipomso ufumu wakumwamba uli ofanana ndi khoka loponyedwa m’nyanja ndi kusonkhanitsa pamodzi zonse zamitundu yonse ; limene podzala analibvuulira pa mtundu; ndipo mmene anakhala pansi anazisonkhanitsa zabwino mzotengera koma zoipa anazitaya kuthengo. Padzatero pa chimariziro cha nthawi ya pansi pano: Angelo adzaturuka adzawasankhula oipa pakati pa a bwino nadzawataya m’ng’anjo yamoto; komweko kudzakhala kulira ndi kukuta mano.

Choncho ufumu wakumwamba ndi “kumwamba” ndiye bwanji? Tikhala nawo bwanji ma fungulo a ufumu wa kumwamba? Werengani nkhaniyi choyamba pa mateyo 13:10-11 “ Ndipo ophunzirawo anadza nati kwa iye chifukwa chanji muphiphiritsa iwo m’mafanizo? Ndipo iye anayankha nati “Chifukwa kwapatsidwa kwa inu kudziwa zisinsi za ufumu wa kumwamba koma sikumapatsidwa kwa iwo.

Kumbukirani mumaphunziro athu a mmbuyo kuti Yesu anadzidzula a ‘Chilamulo’ Chifukwa chobisa mafungulo kuletsa ena kuti alowe? Ndiye apa anawa masulira iwo. Anawalongosolera kuti kuti pali anthu amene mitima yawo ili yoyipitsitsa mwakuti sangamve. Komanso sanalape tsopano iye akukhulupilira mafungulowa a chidziwitso ku mpingo_ _ _ _ _ _ _kwa oyera mtima aliyense.

Onani pa Yuda 3 “ Okondedwa pakuchita changu chonse chakukulemberani za chipulumutso cha ife tonse ndafulumidwa mtima ine kukulembelani ndikudandaulira kuti mulimbanetu chifukwa chikhulupiliro chapatsidwa kamodzi kwa oyera mtima.

Uthenga uli m’manja mwathu. Chidziwitso watipatsa ife ndi mafungulo a ufumu wa kumwamba komabe zilipo zochuluka, Yesu akuyankhula za ayuda kuti ali ndi mafungulo a chidziwitso okha pano akuyankhula zoti akupeleka kwa ife mafungulo a ufumu wakumwamba. Kodi zikutheka bwanji kuti mafungulo a ufumu akuposera mmodzi?

Nzosabvuta. Mafungulowa ndi zifanizo. Ndi mafungulo oti timvetstetse zakumwamba, komanso kulowa kwake, ndi kusalowa kwake, kumwamba. Kumbukirani kuti kupezeka konse kwa “ufumu wa kumwamba” ndi mu Mateyu. Komanso Mateyu akutiuza za mafungulo ku ufumu, ndipo ndi uthenga wa Mateyu yekha umene unagwilitsa mau amenewa mu zifaniziro. Komanso kagawo kena kakupezeka pa mark 4:13 Yesu atango maliza kunena za fanizo la ofesa ( Komanso likupezeka ku Mateyu ndi Luka) Atamaliza ophunzira ake anamfusa kuti zikutanthauza chiyani. Iye anawayankha motere “ Simudziwa kodi fanizo ili? Mukazindikira bwanji mafanizo ena? Yesu akuwauza kuti fanizo limodzi limeneli mfungulo ku mafanizo onse. Ndiye ngati mafanizo ali mafungulo ndiye tiyenera kumvetsetsa fanizo ili la ofesa. Limenero ndilo phunziro likubwera.

Lesson Index