Soldier of Christ Disciple Training Ministries
A ministry of Acts III Global Ministries – USA & Malawi – www.God.mw

CHIYAMBI CHA TCHIMO

Kuyambira pa chiyambi pali zinthu zitatu zimene Yehova wakhala akupitiliza 
I. Kutionetsa ukulu wake pachilengedwe
II. Watidziwitsa zomwe zimayenera kuti chitikira
III. Kutidziwitsa za madalitso posunga malamulo ake ndi chiweluzo pophwanya malamulo ake

TCHIMO LOYAMBA
Kodi uchimo unadzabwanji? Ambiri timayetsa kuti anayamba ndi Adamu/va koma sichoncho. Kale Adamu ndi Eva asanachimwe, uchimo unapezeka kumwamba chimodzi cha zolengedwa modabwitsa, mngelo wamkulu Lucifala, thanda, inapezeka ndi kusakhulupirika taonani mmene analili okongola Eze 28:12-14. Chidzindikiro cha ungwiro, udzala ndi mzeru wokongola’. Unali MEden, mmunda wa Mulungu, mwala uliwonse wamtego wache unali chofunda chako, Sardiyo topazi diamoni, berulo, Sohamu, ndi Yaspi, Safiro nofiki bareketi ndi golidi Malingaka ako ndi akazi ako anakukonzekeratu’. Onalidi mkerubi odzondewda wakuphimba ndipo ndinakuika unali pa Phiri lopatulika la Mulungu, Anayenda yenda pakatipa miyala yamoto’ Unali waungwiro mnjira yako chitengedwere iwe mpa chinapezeka mwa iwe chosalungama.

Tikuona mbali ya tchimoto pa vs 17” unadzikuza mtima wako chifukwa cha kukongola wa ipsa mzeru zako. Komanso tikupeza chosalungama Yesaya 14:12-14 wagwadi kuchokera kumwamba iwe nthanda mwana wa mbanda kucha! Wagwetsedwa pansi iwe ulefuka amitundu “koma unati muntima mwako” Ndizakwera kumwamba ndizakweza mpando wanga wachifumu pamwamba pa nyenyezi za Mulungu ndidzakhala nga wa mwambamwabwayo.

Chilichonse chimene chinalengedwa ndi chabwino. Mulungu sanalenge satana, analenga Lucifala, malingana ndi malemba;
* Wangwiro
* Wa mzeru ndi wokongola
* Thupi lake lokongola kuposa miyala ya mtengo wa patali
* Anali ndi ntchito yayikulu komanso ulamuliro kumwamba
* Anali ndi kuthekera konse pomfikira Mulungu
* Anali opanda tchimo

Koma chinachake chinachitika. Lucifala anadziona ekha, anachoka pa maso pa Mulungu, ndi kumaona kukongola kwake, nzeru ndi mphavu. Sanakhutire kukhala otumikira Mulungu, koma amafuna kukhala Mulungu. Amafuna ufumu wake kuposa wa mulungu, komanso anatsogolera 1/3 ya angelo kuwukira. Yehava anamuweluza Lucifala ndi angelo ake kuchoka ku mwamba.

UCHIMO WA MUNTHU
Mulungu atalenga Adamu ndi Hava, anadzala munda pafupi ndi Edeni. Umo anadzala zomera zonse zoyenera kudya munthu, komanso zokongola. Komanso mitengo iwiri yapadera. Wamoyo, komanso mtengo wachidziwitso pa chabwino ndi choyipa atamaliza anayika munthu ayang’anire. Komanso lamulo limene Mulungu ampatsa pa Gen 2:16-17 Yehova anamulamula munthu, kuti “Mitengo yonse yamunda mudye koma mtengo wakudziwitsa chabwino ndi choyipa umenewo musadya chifukwa tsiku lomwe udzadya umenewo udzafa ndithu. Tsono munthu anali ndi dziko lonse kulilamulira mmene angafunire komanso lamulo limodzi, Usadye chipatso cha ntengo umodzi mmunda onse. Tiyenera kudziwa kuti pamene Mulungu amapeleka lamulo Eva kunalibe, koma Pa Gen 3 tikuona izi 

I. Tsopano njoka inati kwa mkazi Ea!! Kodi anati Mulungu usadye mitengo yonse ya mundamo?
II. Mkaziyo anati kwa njoka “zipatso za mmundamu tidye koma chipatso cha mtengo wapakati pa munda, Mulungu anati musadye umenewo kapena kukhudza mudzafa
III. Njoka inati kwa mkazi “Kufa simudzafa”!
IV. Chifukwa Mulungu akudziwa kuti tsiku limene mukadya umenewo adzatsegu maso anu ndipo mudzakhala ngati Mulungu odziwa chabwino ndi choipa
V. Pamene mkazi anaona kukongola kwa mtengo ndipo unali olakika mmaso komanso opatsa nzeru, anatenga zipatso ndi kudya komanso kumpatsa Adam kuti naye adye
VI. Ndipo maso awo onse anatseguka, ndipo anadziwa kuti ali amaliseche ndipo anasoka masamba a mkuyu kuti adziphimbe

Tiyeni tione zoonjezera izi polingalira pamwambapa;
I. Mu vesi 1 satana akuyesa Eva kuti awone ngati akudziwa zimene Mulungu ananena komanso mau a Mulungu. Ndiye anatembenuza mau a Mulungu “mtengo uliwonse”
II. Tidziwe zimene Eva akudziwa. Anati “Ea tingadye mitengo yonse mmundawu”
III. Pa vesi 3. Akumpangitsa kukhala osamvetsetsa. Iye anati “chipatso cha mtengo wa pakati, Mulunga anati tisadye kapena kukhala, tidzafa. Talingalilirani zimene Adamu anauzidwa ndi Mulungu “koma pa mtengo wa chidziwitso chabwino ndi choyipa musadye pakuti tsiku limenelo mudzafa ndithu.

Tione Hava :
a. samadziwa dzina la mtengo ngakhale komwe unali
b. Ananena kuti asadzaugwire kapena kukhudza adzafa-Mulungu sananene choncho chifukwa chiyani Hava ndizifukwa kuti ayese. Akuti, afanana ndi Mulungu ndi kudziwa zonse. Akumutsimikizira kuti Mulungu safuna kuti akhale ngati iye. Ndichifukwa chiyani satana anagwilitsa ntchito mayeselo amenewa osati ena, tiyeni tione.

Hava anayandikira mtengowo. Anaona; (a) unali wabwino kudya (b) owoneka bwino, wopatsa nzeru, ndimmene njoka inamuuza, ndiye anauyandikira ndi kuugwira , taonani sanafe. Anadzala ndi mphamvu, ndikulawa, sanafe. Ndipo anafuna kugawana tchimo lake ndi Adamu amene anali naye pompo, ndiye poti sanafe kuthupi, nayenso anadya.

Pano pali malingaliro pa umunthu ndi zimene zinalembedwa pa zimenezi. Hava panalibe pamene Mulungu analamula Adamu, za chipatso choletsedwa. Ndiye amayenera kuuzidwa ndi Adamu. Koma Adamu anali odzikweza, chifukwa Mulungu asanalenge Hava, analenga nyama zonse ndi kuti Adamu anene maina. Anapatsidwa ulamuliro wotchula maina onse. Kenaka Mulungu analenga Hava kuchokera kwa Adamu ndipo yekhayo anapatsidwa dzina.

Pano tili ndi Adamu monga oyang’anira dziko ndi mkazi wake amene Mulungu anampatsa Adamu anayenera kuwonetsetsa kuti Hava asalakwitse pa kudya chipatso choletsedwa ndiye anamuuza iye zina monga izi “Hava waona mtengo uwo pakato pa munda”? usayandikire. Mulungu anati tikadya kapena kukhudza tizafa. Mwina adamu amaona kuti Hava samakhulupilira kuti choonadi. Kapena zimene zinamuonetse Hava kukhala otsika komanso osamva poyelekesa Adamu mwina pokunva kuti adzafanana ndi Mulungu kapena satana anali kuona mmene Adamu amamutengela mkazi wake, ndikudziwa chimene angagwere. Choncho tisaonjezere kapena kuchotsera pa mau a Mulungu chibvumbulutso 22:18-19. Koma Adamu analipo pamene Hava amachimwa. Mwina amaganizira kuti akafa Mulungu apangira wina. Koma pamane asanafe nayenso anadya. Ndichifukwa chake malemba amanena kuti Hava ananamidzidwa koma Adamu anachimwa. Ndi amene anaudzidwa ndi Mulungu. Hava ananamizidwa ndi Adamu komanso njoka. Mwaichi malemba amanena kuti tchimo linadza chifukwa cha Adamu osati Hava. Malo abwino kubweretsa Yakobu 3:1 musakhale aphunzitsi ambiri abale anga podziwa kuti tidzalangika koposa.

Mau oti mphunzitsi tingawamasulire kuti atsogoleri. Tonse tiyenera mayitanidwe anthu monga Abambo, Amayi oyang’anira panyumba, makamaka azitsogoleri, abusa avangeli kumpingo.

Pomaliza maso awo anatseguka, kuuchimo wawo, anafulumila kuyesa kuphimba uchimo ndi tchito ya manja awo posoka masamba a mkuyu.

Pamene Mulungu akuyenda mmunda akuyitana munthu osamuona, Mulungu saona tchimo. Anali atafa pamaso pa Mulungu. Tsiku lomwe anachimwa anafa kwaiye tsiku limenero Mulungu amayenera msembe yamwazi kwa iye mwini. Pokwanilitsa dongosolo la kukhululukira kwa tchimo nthawi zonse.

Mwana aliyense oyamba kubadwa amayenera kuphedwa pofuna kuchotsa machimo, ntchito zawo za chilungamo, zovala zawo, sizinali zokwanira. Ngakhalenso ntchito zathu sizokwanira kuchotsa litsilo la ntchimo

Lesson Index