Soldier of Christ Disciple Training Ministries
A ministry of Acts III Global Ministries – USA & Malawi – www.God.mw

UCHIMO NDI ZOVUTA

Kungolingalira uta ndi mumvi, utakokedwa kwambiri. Ndiye mwaganiza zoponyera m’mwamba pagulu la anthu choncho mwaponya. Kenako mwaona kuti ndi zopusa ziminezo, ngakhale simumafuna kubaya wina koma mumvi potsika pansi wina ayenera kuvulala mwina oyandikana nanu. Kenako mwagwada ndikupephera zonse zimene mukufuna koma mwazindikira kuti mumvi tsopano simungathe kuwutenganso uyenera kuononga basi. Pamenepo mukhala m’mavuto basi monga mwa fanizo la mumvi, choopsa kwambiri timachiona m’malemba ndi chakuti ntchimo silikhudza moyo wathu wokha koma iwo amene tiwakonda amene tiyanjana nawo ngakhale osadziwa. Zotsatira za tchimo zilingati mwala oponyedwa pa dawu la msomba sichiphokoso chokha koma mafundenso. Komanso chamoyo chilichonse chikhuzidwa. Mwachoncho machimo athu samangokhudza ife tokha. Tiyeni tione malemba amene akuonetsa pamene machimo amafika.

ADAMU – IMFA PA DZIKO LONSE (KWA ANTHU)
Baibulo limati chifukwa cha Adamu, munthu aliyense amabadwa ndi uchimo taonani mmusimu. Chifukwa Adamu anaswa lamulo limodzi kuti tikalowe kumwamba tiyenera kuyamba tafa. Tchimo laka silinakhudze iye mwini yekha.  Onani pa Aroma 5 vs 12---18 komanso pa 1Akolinto 15 vs 22

HAMU – ANATEMBELERA ANA AKE 
Nowa anali ndi ana atatu, chitatha chigumula nowa anadzala mpesa. Kuchokera mumpesa anaphika mowa. Pa tsiku iri anledzera kwambiri ndipo anali wamaliseche kenako Hamu, analowa ndi kuona umaliseche wa a bambo wake, atuluka kuuza azibale ake omwe analowa cha m’mbuyo ndikufunda atate awo. Hamu anapeputsa abambo wache. Pamenepo Nowa anadzuka ndidziwa chimene Hamu anachita sanamutembere koma anatemberera kanani mwana wa Hamu. GENESIS. 9:18-27
Zotsatira za temberero kuyambira nthawi ya Nowa, ana a kanani anavutitsidwa ndi Israel. Malo amene amakhala ndi olonjezedwa ku ana a Abraham malowa amayenera kugawidwa kumafuko 12 a Israel. Chifukwa cha mwano wa Hamu ana ake akuvutika kwa zaka zambiri. Akanani – Dziko lake linaluza nkhondo, asilikali ndi mabanja ake anafa pamene Yoswa anatsogolera anthu ake kudziko la lonjezano, anaphwasula mpanda wa Yeriko. Koma, Mulungu anawalamula kuti siliva ndi golide ziyenera kupita kwa Yehova. Onani Yoswa 6: 18-19
Choncho Aisaraeli, kudzera mu mphavu ya Yehova anagwetsa yeriko popanda vuto. Komanso amayembekezera kugwetsa mzinda wa Ai. Tione dongosolo: Yoswa 7: Choncho iyi inakhala nkhondo yophweka kwa Isaraeli. Koma kunkhondo? Yoswa 7: 4-5.Akhondo amphavu a Isaraeli anakathidwa. Anthu 36 anaphedwa. Mitima ya anthu inachita matha ndi ka mzinda kakangóno chifukwa? Yoswa amafuna kudziwa. Anangámba zovala, nkhope pansi ndikulira mayankho. Mulungu anati taonani zimene yehova anyankha Isaraeli wa chimwa. Isaraeli wa phwanya malamulo anga. Chifukwa cha machimo awo sangagonjetse adani awo. Adzatembenukira kumbuyo ndikuthawa. Akudzudzulidwa. Mulungu sadzakhanso kumbali yao. Kuti Mulungu akhalenso kumbali yawo ayenera: kuphwanya chimene chiswa lamulo. Aliyense adzikhuthule. Mwawalaka, Yoswa afufuza amene waswa lamulo kuyambira pa mafuko 12. Kenaka oyangánira mabanja mpaka anapeza akanani ndikumuuza kuti alape ndipo anauza anthu pamene anabisa zithu. Akanani anayimbidwa milandu, pano pali chiweluzo Yoswa 7: 24-26. Tchimo la akanani, Isaraeli analuza nkhondo. Anthu 36 anafa. Akanani ndi ana ake, ziweto zake ndi zonse anali nazo zinaotchedwa ndi moto. Tchimo linaphetsa anthu osalakwa. Mfumu Davide pa ziweluzo zitatu anachenjedwa ndi Mulungu kuti asawerenge anthu mavuto anayamba. Yoabu anadzawa kuti kuchimwa Davide sikudzakhala kwa Yekha koma dziko lonse koma Davide sanamvere anapitiliza chiwerengero cha anthu pa versi ya 7 ikuti: koma sizinali zophweka kudzichita. Mulungu anyakhula ndi Davide kudzera mneneri Gadi. Mulungu anapereka ziweluzo zitatu patchimo lake 1 mbiri 21: 11-12. Chisankho cha Davide pa tchimo lake zaka zitatu za njala pa dziko lonselo. Mwezi itatu yakuthedwa pa adani ako ndi lupanga. Masiku atatu a lipanga la yehova kuphatikiza muliri ndi angelo owononga a yehova kudzaononga Isaraeli. Davide anasakha kuyika vutoli mmanja mwa mulungu osati munthu. Choncho anthu 70,000 osalakwa anafa ndi nthenda, chifukwa cha tchimo la Davide. Amenewa anali anthu amene anawerengedwa kuti aone kukula kwa gulu la nkhondo akufuna kuliyitana. Izi ndi zina ndi zina mwa zimene anthu osalakwa amavutika chifukwa cha tchimo la wina. Alipo malemba ambiri zosakoma kwa munthu koma kwa yehova akusunga mawu ake pa Ex 34: 6-7. Tiyenera kuzindikira kuti machimo athu amatipitilira ife eni. Amakhudza onse otiyandikira, maka lero mu nthawi ya mpingo. Mpingo ndi thupi zilibe kanthu kuti wavulala pati thupi lirilonse limadwala. Pakhonza kukhala m’manso, pakamwa, pakhungu. Koma ngati zikubweretsa nthenda, thupi lonse limadwala. Chimodzimodzi tchimo. 

Lesson Index