![]() |
Soldier of Christ Disciple Training Ministries |
|
Lesson 103 |
|
| Ndidzakupatsani mafungulo (makiyi) a ufumu wakumwamba. Ndipo chimene ndikamanga padziko lapansi chidzakhala chomangidwa kumwamba : Ndipo chimene ukachimasula padziko lapansi chidzakhala chomasulidwa kumwamba. “ Mateyu 16:19. Taona kale kuti kumanga kulibe ntchito pa mdierekezi. Muphunziro lathali, taphunzira kuti kumanga ndi kumasula ndiko khudzana ndi kuyika china chake mugoli la lamulo. Kapena kumasula kuchokera ku chilamulo. Komanso tinaona ena kuti imfa ndiyo njira yokhayo yomasulidwira. Tikakaonanso kumbuyo pa mau ofunika, tikukhalabe ndi ‘makiyi’ ndi ‘ufumu wakumwamba’ phunziro iri likhala likuunika za Makiyi (mafungolo). Choyamba makiyi ndi chiyani? Chabwino, yankho lophweka ndi lakuti, ndi chida chotsekulira chinthu chokiyidwa. Atha kukhala makiyi otsekulira loko kapena atha kukhala mau ofunikira omasulira chining’a. ndiye tiyeni tione ‘makiyi’ akugwilitsidwa mmalemba. Mau oti mafungulo (makiyi) agwilitsidwa kawiri, Mateyu 16:19. Komanso pa Chibvumbulutso 1:18 Yesu anati ndine amene ndiliwamoyo ndipo ndinali wakufa ndipo taona ndiri wamoyo kufikira nthawi zanthawi ndipo ndiri nazo zofungulira za ifa ndi hade. Mau oti ‘mfungulo’ agwilitsidwa ntchito kasanu ndi kamodzi mmalemba, koyamba pa yesaya 22:22 “Ndipo ndidzaika mfungolo wa nyumba ya Davide paphewa pache ndipo iye adzatsegula ndipo palibe adzatseka, Iye adzatseka ndipo palibe wina adzatsegula. Uwu ndi uneneri okhudza mesiya-Yesu Adzakhala ndi mafungolo a nyomba ya Davide –Moyo osatha. Tikuonanso pa Chibvubmulutso 3:7 ndipo kwa mngelo wa mpingo wa ku Filadelfya lemba. Iye amene ali woyera, amene ali woona, Iye wakukhala nacho Chifungolo cha Davide Iye wotsegula ndipo palibe wina atseka, Iye wotseka palibe wina wotsegula…. Tikupezanso “Mfungulo” Pa Luka 11:52 “Tsoka inu achilamulo! Chifukwa munachotsa chifungulo cha nzeru; inu simunalowamo nokha ndipo mwaletsa iwo analinkulowa Yesu akuyankhula kwa iwo odziwa chilamulo cha Mose, osati chilamulo chadziko. Tsona zomwe taona za ntchito ya mfungulo, komanso mafungulo mmalemba; - Tikufunafuna mafungulo a ufumu wakumwamba - Yesu ali ndi mafungulo otsegulira ndi kutseka zitseko ndipo palibe wina angathe. Akatseka sitingatsegule ndipo akatsegula sitingatseke. - Anthu a chipembedzo a munthawi ya Yesu – Mlembi, Afalisi ndi Asaduki-Anadzudzulidwa ndi mkhristu chifukwa chochotsa mafungulo a nzeru mafungulo chidziwitso amenewa , amatsegula khomo,lolowera penapake, pamene anachotsa mafungulo a chidziwitso Amalepheretsanso ena kuti alowe. Ndiye ndikufuna kuti ndinene kuti mafungulo angakhale otani sangathe kutsegula chimene yesu Watseka komanso sangathe kutseka chimene yesu watsegula. Komanso pakuti Ayuda analetsedwa ndiye mwina Ambuye akufuna kutipatsa mafungulo a chidziwitso amene akatsegula khomo kwa ife kuti tipite kulikonse. Komabe tikusoweka kudziwa mafungulo achidziwitso komanso kuti amatsegula chiyani? Komanso kuti zimenenzi zikukhudzana bwanji ndikumanga ndi kumasula? Kodi ndizoyenera kunena kuti mafungulo aliwonse a nzeru amene ayuda analinawo anadzanso ndi mphamvu yomanga ndi kumasula? Talingalirani Yesu anati: 1) Atenga mafungulo anzeru. 2) Osalowa paliponse pamene mafungulo achidziwitso amatsegula. 3) Analetsa ena kuti asalowemkati. Kodi ndi zoyenera kunena kuti mafungulo a nzeru za Ayuda anadza ndi mphamvu yo masula Anthu komanso yowalora kulowa pena paliponse pamene iwo amayera kulowa kapena kumanga iwo, powaletsa kulowa pamalo amenewa? Ndiye zikuoneka kuti mafungulo a nzeru ya Ayuda apatsidwe tsopano kwa oyeramtima, komanso kuti amatsegula makomo a ufumu wa kumwamba. Muphunziro likudzali tidzaona ndime yomaliza tisanaphatikize zones limodzi. |
|