Soldier of Christ Disciple Training Ministries
A ministry of Acts III Global Ministries – USA & Malawi – www.God.mw

Lesson 105

‘Simudziwa kodi fanizo ili? Mukazindikira bwanji mafanizo onse’ Mark 4:13

Fanizo limeneli la ofesa likupezeka mu mauthenga abwino atatu. Koma uthenga uliwonse ukuwonjezera timfundo pang’ono. Ndiye pofuna kusunga malo ndaphatikiza atatu onse popanda kusintha chilichonse. Ndiye fanizoli likuchokera pa Mark 4:3-9, Luka 8:5-8 ndi Mateyu 13:3-9. Ndiye pano taphatikiza.

Ndipo ofesa anaturuka kukafesa, mkufesa kwake, zina zinagwera m’mbali mwanjira, ndipo zinapondedwa ndimapazi komanso mbalame za mulengalenga zinadya izo. Zina zinagwa pa nthaka yathanthwe pamene panalibe nthaka yambiri, ndipo nthawi yomweyo zinamera chifukwa zinalibe nthaka yambiri. Ndipo zitakula, dzuwa litakwera zinapselera ndipo popeza zinalibe mizu ndi chinyezi zinakwinyata. Mbeu zina zinagwera pa minga ndipo minga inakula nizitsamwitsa ndipo sizinabala zipatso. Ndipo zina zinagwera pa nthaka yabwino ndipo zinapatsa zipatso ndi kukula ndi kuchuluka ndipo zinabala kupindula makumi atatu ndi makumi asanu ndi limodzi ndi makumi khumi.

Ndiye ife tisanawonjezere apa tiyeni tiwone mmene Yesu anafotokozera fanizo limeneri. Komanso kafotokozedwe kake mmauthenga onse atatu aphatikizidwanso kuchokera pa Mark 4:14-20, Luke 8:11-15 ndi Mateyu 13:18-23

‘Ndipo ananena nao.’ Simudziwa kodi fanizo ili? Mukazindikira bwanji mafanizo onse? Tsopano nali fanizoli: ofesa anafesa mbeu, ndipo mbeu ndi mau a Mulungu. Izo zam’mbali mwa njira ndi anthu amene anamva mau a ufumu wakumwamba koma sanamvetsetse, ndipo mdyerekezi amadza nthawi yomweyo ndikuwalanda mau amene afesedwa mutima mwawo kuti asakhulupirire ndi kupulumutsidwa munjira yomweyi izo zogwera panthaka ya thanthwe ndi anthu omwe anamva mau ndikuwalandira ndi chimwemwe, ndipo chifukwa alibe mizu yeniyeni iwo ndiosakhalitsa ndipo pakafika zokhumudwitsa ndi mayesero chifukwa cha mau amakhulupilira kwa kanthawi ndipo chifukwa cha mau, nthawi yomwe amagwa Mbeu yogwera pa minga, awa ndi anthu amene anamva mau koma alimumau omweyo anatsamwidwa ndi madandaulo adziko lapasi,kunamizidwa ndi chuma komanso zosangalatsa za moyo uno, ndipo mau amakhala osabala zipatso ndipo palibe chipatso chomwe chinakwima. Koma mbeu ya pa nthaka yabwino awa ndi anthu amene anamva mau ndi mtima woona ndi kuwasunga ndi kuwagwilitsitsa ndi kubala zipatso ndi chipiliro ndi kubweretsa zokolora zina makumi asanu ndi limodzi ndi makumi khumi zina makumi atatu.

Tsopana tiyene tizifunse mafunso ochepa kuti timvetsetse fanizoli ndi kulongosoledwa kwake.
  1. Kodi zikuthatauza chain? –Zosabvuta fanizoli likukamba za chipulumutso choona ndi chonyenga likuphunzitsa ife kuti tikathe kuzindikira otembenuka mtima enieni ndi achinyengo kuwonjezera apo ndi uthenga komanso chenjenzo kwa akhristu owona m’mene angafalitsile mbeu. Zomwe zitalongosoledwe bwino bwino.
  2. Kodi ofesa ndi ndani? Ofesa ndi Avangeli, Azilaliki komanso munthu wina aliyense amene amagawa uthenga (Kapena gawo lina la uthenga) kwa otayika. Ndi nkhani ya nkhani kwa ofesa monganso kwa otayika. Ifeyo ndi amene timatenga mau a mulungu ndi kuwamwaza penapaliponse.
  3. Kodi nthaka zosiyana siyanazi ndi ndani? Nthaka zinai zosiyana siyanazi ndi anthunso anayi osiyana malingana ndi mitimayo. Anthu amenewa akusiyana malingana ndi mmene alandirila mau a Mulungu. Zomwe titabvundukule pano ndizoti ena alindi mitima yowuma yosakozekera kulandira mau. Ena amamva nthenga osatsilizika(osamalizika) bwino ndipo gulu la chitatu limamva uthenga onse bwino koma osazindikira mtengo wake ndipo gulu la chinayi lima mvetsetsa ndi kukhala muuthenga wabwino.
  4. Kodi ife zikutiuza chiani? Kwa ifenso zikutengera gulu lomwe ifeyo tili ena mwa ife ndife otayika ndipo tikufunika kulandira uthenga. Ena akudzinyenga okha komanso kukhala mchinyengo ndipo mwa iwo choonadi mulibe. Amenewa ayenera kulingali iwo eni. Enanso amene akubala zipatso ayenera kuzindikira kuwopsa kwa uthenga osathililidwa kuti akathe kuwonjezera zokolola komanso kuti asakakhale zophuthwitsa panjira ina iliyonse
  5. Kodi fanizoli lingamasule bwanji ma fanizo ena onse? Zomwe titaone ndizakuti zifanizo zina zones zikukamba za nkhani yake yomweyi-------kusiyanitsa kwa zeni zeni ndi zachinyengo. Mumafaniziro ambiri omwe ali mbaibulo timangolingalira kuti amakamba za kusiyana kwa anthu otayika ndi opulumutsidwa. Koma tikalimvetsetsa fanizoli koyamba tizindikira kuti zifanizo zina zones zikukamba za pakati pa ana eni eni a Mulungu ndi ana a chinyengo a Mulungu.

Tsopano tiyeni tione ngati tingazindikire kufunikira kwa mafungulo ku zifanizo zonse. Tiyamba kuona gulu ndi gulu pophatikiza ndi kulongosola kwa Yesu monga zalembedwa pamwmbapa.

Lesson Index