![]() |
Soldier of Christ Disciple Training Ministries |
|
MAFUNGULO A UFUMU WAKUMWAMBA - 106 |
|
| Fanizo la ofesa- Gulu 1- Mbeu za mmbali mwamseu fanizo: Ofesa anatuluka kukafesa mbeu, ndipo akufesa zina zinagwera mmbali mwanjira , ndipo zinapondedwa ndi mapazi komaso mbalame za mulengalenga zinadya mbeuyo. Kulongosola kwa Yesu: Ofesa anafesa mbeu, ndipo mbeu ndi mau a mulungu. Ndipo mbeu yogwera mbali mwanjira ndi anthu amene amamva mau a a fumu wakumwamba koma osawamvetsetsa. Ndipo nthawi yomwe satana amabwera ndi kutenga mau amene afesedwa mutima mwao kuti asakhulipilire ndi kupulumutsidwa. Kulingalira kwambiri: Anthu amene Yesu akuwanena pamenepa anawalongosolerakale pamene iwo anafunsa chifukwa chimene iye amaphunzitsa muzifanizo taonani yankho lake lalitali pa mateyu 13:11-17 “Ndipo Yesu anayankha nati” Chifukwa kwapatsidwa kwa inu kudziwa zinsinsi za ufumu wakumwamba koma sikunapatsidwe kwa iye, ndimo adzakhala nazo zochuluka koma yense amene alibe chingakhale chomwe alinacho chidzachotsedwa kwa iye chifukwa chache ndiphiphiritsa iwo m’mafanizo chifukwa kuti akuona samaona ndi akumva samamva kapena samadziwa. Ndipo anakwanilitsidwa kwa iwo mau adanenera yesaya, amene anati:- Pakumva mudzamva ndipo simudzazindikira konse, Pakupenya mudzapenya ndipo simudzaona konse chifukwa unalemera mtima wa anthu awa ndi m’makutu ao amamva mogontha, ndimaso ao anatsinzina kuti asaone konse ndimaso asamve ndi makutu, asazindikire ndi mtima wao asatembenuke ndipo ndisawachilitse iwo. Koma maso anu ali wodala chifukwa apenya; ndi makuti anu chifukwa amva. Pakuti ndetu ndinena kwa inu kuti aneneri ambiri ndi anthu olungama analakalaka kupenya zimene muziona koma sanaziona ndi kumva zimene muzimva, koma sanazimva. Yesu anatenga mau a mneneri Yesaya 6:9-10 zokhudzana ndi anthu amene analowelera mu uchimo komanso kutaya malamulo a Mulungu komanso mau a Yesaya malamulo a Mulungu komanso mau a Yehova. Mwakuti Mzimu wao watha makutu awo agontha ndi maso awo sangathe kuona Yehova,chilamulo, komanso chikhalidwe chawo chifukwa cha uchimo. Komanso tikupeza nkhani yomweyi pa Masalimo 119:70 “Mtima wawo unona ngati mafuta koma ine ndikondwera nacho chilamulo chanu” Ichi chinali chodziwikiratu mu dziko la Yuda. Aneneri onse komanso mauthenga onse. Taonanso apa kuchokera pa Zakariya 7:11-12 “ Koma anakana awo kuti asamve inde anasanduliza mitima yawo ikhale ngati mwala woti gwa, kuti angamve chilamulo, ndi mau a Yehova wa makamu anatumiza ndi mzimu wache mwa aneneri oyamba aja mmenemo munafuna mkwiyo waukuru wochokera kwa Yehova wa makamu. Bvuto limeneli logontha mmakutu ndi kukhala ndi nthenda mmakutu a uzimu siyochepa mu chipangano chakale Yesu amaphunzitsa za mabvuto amene amapezeka munthawi ya mpingo. Taonani pamene akuti mbeu inapondedwa ndi mapazi. Wina aliyense amene wayeselapo kugawa uthenga ndi wina wake angabvomelezane ndi nkhaniyi_ _ _ _ _ _mwina kutonzedwa kapena kuonetsa kupanda chidwi ndi uthenga. Mwina awa ndi amene Yesu anawa kamba pa Mateyo 7:6 pamene iye anati “Musamapatsa chopatulikacho kwa agaru ndipo musamaponya ngale zanu patsogolo pa nkhumba kuti zingazipondeleze ndi mapazi awo ndi potembenuka zingang’ambe inu. Toana akugwilitsa ntchito mau omwewa,_ _ _ _ _ _kupondedwa ndi ngati mapazi. Izi sizikuthathauza kuti tikhale ngati Yona kuti tokha tidziganizira iwo amene akuyenera chipulumutso, koma tiyenera kugawa uthenga mmene ambuye angatitsogolere kudzera mu mzimu wake. Tinakakhala ndi mwayi oti mbeu zimere munseu kusiyana ndi mbeu yomera mu mtima mwa munthu ngati ameneyu. Anthu amenewa Sali okozeka kulandira ngakhale kumva uthenga. Takamuona mvangeli_ _ _ _ _ _ ofesa kuponya mbeu mumbali mwa njira ndiye kuti ndi wa ulesi komanso njira yosabvuta. Tikuyenera kuchoka munjira ndikulowa mutchire kusaka nthaka yabwino. Izi zingapangitse ubale ndi munthu kuti mzimu ungagwiritse ntchito inuyo kuyamba kugalauza mmitima yawo kuti akalandire mbeu munthawi yakudzala. |
|